37 Zimenezi ndi zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza monga misonkhano yopatulika+ yoperekera nsembe zowotcha pamoto kwa Yehova. Imeneyi ndi misonkhano yoperekera nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ motsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku.