9 Muziwerenga masabata 7. Muziyamba kuwerenga masabata 7 amenewo kuchokera pa nthawi imene mwayamba kumweta tirigu.+ 10 Ndiyeno muzichitira Yehova Mulungu wanu Chikondwerero cha Masabata,+ popereka nsembe zaufulu zimene mungathe, mogwirizana ndi mmene Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.+