10 Nehemiya anati: “Pitani mukadye zinthu zabwino kwambiri, mukamwe zokoma ndiponso mukagawire chakudya+ anthu amene alibe, chifukwa lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Musadzimvere chisoni, chifukwa chimwemwe chimene Yehova amapereka ndi malo anu achitetezo.”