-
Luka 21:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+ 3 Ndipo iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu, waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama zawo.+ 4 Chifukwa onsewa aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+
-