3Mose anakhala mʼbusa wa ziweto za Yetero*+ apongozi ake, wansembe wa ku Midiyani. Pamene ankaweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona, ku Horebe.+
1Yehova analankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai,+ mʼchihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri mʼchaka chachiwiri, atatuluka mʼdziko la Iguputo.+ Iye anati: