-
Numeri 16:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Kenako Kora+ mwana wa Izara,+ mwana wa Kohati,+ mwana wa Levi,+ anagwirizana ndi adzukulu a Rubeni,+ omwe ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliyabu,+ komanso Oni mwana wa Pelete, kuti aukire. 2 Iwo limodzi ndi amuna a Chiisiraeli okwana 250 anaukira Mose. Amunawa anali atsogoleri a anthuwo, amuna osankhidwa pakati pa Aisiraeli, amuna otchuka.
-