15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu. 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo akumabwera nawo kwa ine, ndipo ndikumaweruza nʼkuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+
11 Mnyamatayo anayamba kunyoza* ndi kutukwana dzina la Mulungu.*+ Ndiye anapita naye kwa Mose.+ Dzina la mayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri wa fuko la Dani. 12 Ndiyeno anamutsekera kudikira kuti Yehova apereke chigamulo pa nkhaniyo.+