16 Mayina a ana aamuna a Levi,+ mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo ndi awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137.
57 Tsopano awa ndi mayina a amuna amene anawerengedwa pakati pa Alevi+ potengera mabanja awo: Agerisoni, a banja la Gerisoni, Akohati, a banja la Kohati+ ndi Amerari, a banja la Merari.