-
Numeri 15:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Komanso popereka nsembe ya nkhosa yamphongo, muzikaipereka limodzi ndi nsembe yambewu yokwana magawo awiri a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. 7 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini, kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
-