-
Deuteronomo 32:48-50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 Yehova analankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49 “Kwera mʼphiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili mʼdziko la Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa Aisiraeli kuti likhale lawo.+ 50 Kenako ukafera paphiri limene ukufuna kukwerali nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako,* mofanana ndi Aroni mʼbale wako amene anafera paphiri la Hora+ nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.
-