-
Yoswa 22:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Mose anali atapatsa hafu ya fuko la Manase cholowa chawo ku Basana.+ Hafu ina ya fukolo, Yoswa anaipatsa cholowa pamodzi ndi abale awo kutsidya lina la Yorodano kumadzulo.+ Komanso pamene Yoswa ankawauza kuti azipita kumatenti awo, anawadalitsa. 8 Anawauza kuti: “Bwererani kumatenti anu ndi chuma chambiri, ziweto zambiri, siliva, golide, kopa, zitsulo ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munakatenga+ kwa adani anu ndipo mukagawane ndi abale anu.”
-