13 Mbali yotsala ya dera la Giliyadi ndi Basana yense amene anali mu ufumu wa Ogi ndinaipereka kwa hafu ya fuko la Manase.+ Dera lonse la Arigobi, limene ndi mbali ya Basana linkadziwika kuti ndi dziko la Arefai.
31 Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti, Edirei+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi mʼdziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri motsatira mabanja awo.
17Kenako fuko la Manase,+ mwana woyamba wa Yosefe,+ linapatsidwa gawo lake.+ Makiri+ mwana woyamba wa Manase, bambo wake wa Giliyadi, anali msilikali wamphamvu, choncho anapatsidwa dera la Giliyadi ndi Basana.+