36 Choncho ana a Loti awiri onsewo anakhala oyembekezera atagona ndi bambo awo. 37 Mwana woyamba anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndi tate wa Amowabu amasiku ano.+
13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.