19 Ine ndinkaganiza kuti, ‘Mosangalala ndinakuika pakati pa ana aamuna nʼkukupatsa dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri pakati pa mitundu ya anthu!’+ Ndinkaganizanso kuti uzindiitana kuti, ‘Bambo anga!’ ndiponso kuti sudzasiya kunditsatira.