15Gawo limene linaperekedwa+ ku fuko la Yuda kuti ligawidwe kwa mabanja awo linkafika kumalire a Edomu+ ndi kuchipululu cha Zini, mpaka kumapeto kwa Negebu, kumʼmwera.
3 Malirewo analowera kumʼmwera kuchitunda cha Akirabimu+ nʼkukafika ku Zini. Kenako anakwera kuchokera kumʼmwera kupita ku Kadesi-barinea,+ nʼkukafika ku Hezironi mpaka ku Adara, nʼkuzungulira kukafika cha ku Karika.