11 Koma ngati munthu amadana ndi mnzake+ ndipo wamubisalira panjira nʼkumuvulaza kwambiri mpaka mnzakeyo kufa, iye nʼkuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu amumzinda wakwawo azimuitanitsa kuchokera kumeneko nʼkumupereka mʼmanja mwa wobwezera magazi ndipo azimupha.+