42 Ana a Merari anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo, 43 anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+ 44 Onse amene anawerengedwa mogwirizana ndi mabanja awo anakwana 3,200.+