-
Ekisodo 18:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu.
-
-
Numeri 15:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Amene anamupeza akutola nkhuniwo anapita naye kwa Mose ndi Aroni ndiponso kumene kunali gulu lonselo.
-
-
Numeri 27:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewa mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 2 Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, wansembe Eleazara, atsogoleri+ komanso gulu lonse, pakhomo la chihema chokumanako nʼkunena kuti:
-