15 Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Pa tsiku loyamba muzichotsa mʼnyumba zanu ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa chifukwa aliyense wodya mkate wokhala ndi zofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7, munthu wochita zimenezi aziphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli.