-
2 Mbiri 7:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ansembe anali ataimirira pamalo awo a ntchito. Nawonso Alevi anaimirira pamalo awo ndipo ananyamula zipangizo zoimbira Yehova nyimbo.+ (Mfumu Davide anapanga zipangizo zimenezi kuti azizigwiritsa ntchito poyamikira Yehova komanso pomutamanda kudzera mwa iwowo,* “chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”) Ansembe ankaimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.
-
-
Ezara 3:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Anthu amene ankamanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko a kachisi wa Yehova.+ Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe omwe ananyamula malipenga+ ndiponso Alevi, ana a Asafu omwe ananyamula zinganga, anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa.+
-