16 Ndiyeno wansembe wa ku Midiyani+ anali ndi ana aakazi 7. Iwo anafika pachitsimepo kuti atunge madzi ndi kuwathira momwera ziweto kuti ziweto za bambo awo zimwe.
3Mose anakhala mʼbusa wa ziweto za Yetero*+ apongozi ake, wansembe wa ku Midiyani. Pamene ankaweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona, ku Horebe.+
5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, limodzi ndi ana aamuna a Mose ndi mkazi wake, anapita kwa Mose mʼchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+