3Mose anakhala mʼbusa wa ziweto za Yetero*+ apongozi ake, wansembe wa ku Midiyani. Pamene ankaweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona, ku Horebe.+
16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakuta phirilo kwa masiku 6. Pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo.