Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 17:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Zitatero Mose anauza Yoswa+ kuti: “Tisankhire amuna ndipo upite nawo kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona mʼdzanja langa.”

  • Ekisodo 24:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka,+ ndipo Mose anakwera mʼphiri la Mulungu woona.+

  • Ekisodo 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova ankalankhula ndi Mose pamasomʼpamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake Yoswa,+ mwana wa Nuni, sankachoka kuchihemako.

  • Numeri 27:18-20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,* ndipo uike dzanja lako pa iye.+ 19 Kenako umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara komanso pamaso pa gulu lonse, ndipo umuike kuti akhale mtsogoleri pamaso pawo.+ 20 Umupatseko mphamvu zako,*+ kuti gulu lonse la Aisiraeli lizimumvera.+

  • Deuteronomo 31:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni. Iye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu ndipo inu mudzaithamangitsa.+ Yoswa ndi amene akutsogolereni nʼkukuwolotsani,+ mogwirizana ndi zimene Yehova wanena.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena