-
Genesis 46:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli mʼmasomphenya usiku kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”
-
-
Ekisodo 24:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera mʼphirimo, 10 ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake pankaoneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, yoyera ngati kumwamba.+ 11 Mulungu sanawononge atsogoleri a Aisiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona ndipo anadya ndi kumwa.
-