Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 26:65
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 65 Zinakhala choncho chifukwa ponena za iwo, Yehova anati: “Ndithu anthu amenewa adzafera mʼchipululu.”+ Choncho, palibe amene anatsala kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+

  • Numeri 32:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, sadzaliona dziko+ limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12 Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaliona dzikolo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’+

  • Deuteronomo 1:34-38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Nthawi yonseyi Yehova ankamva zimene munkanena ndipo anakwiya kwambiri, moti analumbira kuti,+ 35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mʼbadwo woipa uwu amene adzaone dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune. Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzapereka dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+ 37 (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, “Iwenso sukalowa mʼdziko limeneli.+ 38 Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira+ ndi amene akalowe mʼdzikomo.+ Umulimbitse,*+ chifukwa ndi amene adzatsogolere Aisiraeli pokatenga dzikolo kukhala lawo.”)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena