20 Ndikukutumizirani mngelo patsogolo panu+ kuti azikutetezani mʼnjira komanso kukakulowetsani mʼdziko limene ndakukonzerani.+ 21 Muzimumvera ndi kuchita zimene wanena. Musamupandukire, chifukwa sadzakukhululukirani zolakwa zanu,+ popeza dzina langa lili mwa iye.