-
Levitiko 22:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni amene ali ndi khate+ kapena nthenda yakukha,+ asadye zinthu zopatulika mpaka atakhala woyera.+ Zikhalenso chimodzimodzi ndi aliyense wokhudza munthu amene wadetsedwa chifukwa cha munthu wakufa,+ kapena mwamuna amene watulutsa umuna,+ 5 kapenanso mwamuna amene wakhudza chilichonse mwa zamoyo zodetsedwa zopezeka zambiri,+ kapena amene wakhudza munthu wodetsedwa pa chifukwa chilichonse amene angachititse kuti akhale wodetsedwa.+ 6 Munthu wokhudza chilichonse mwa zinthu zoterezi azikhala wodetsedwa mpaka madzulo ndipo asamadye chinthu chopatulika chilichonse, koma azisamba thupi lonse.+
-