21 Zitatero, Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka Sihoni ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Aisiraeli. Choncho anawagonjetsa nʼkutenga dziko lonse la Aamori okhala kumeneko.+ 22 Anatenga chigawo cha Aamori kuchokera ku Arinoni kukafika ku Yaboki ndiponso kuchokera kuchipululu kukafika ku Yorodano.+