-
Oweruza 11:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi amene anagonjetsa Aamori+ pamaso pa anthu ake Aisiraeli, ndiye iwe ukufuna kuwathamangitsa? 24 Kodi chilichonse chimene mulungu wako Kemosi+ wakupatsa, si chimene umakhala nacho? Choncho aliyense amene Yehova Mulungu wathu wamuthamangitsa pamaso pathu ndi amenenso ife timamuthamangitsa.+
-
-
2 Mafumu 23:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Komanso inachititsa kuti malo okwezeka akutsogolo kwa Yerusalemu omwe anali kumʼmwera* kwa Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti mulungu wamkazi wonyansa wa Asidoni, Kemosi mulungu wonyansa wa Amowabu ndi Milikomu+ mulungu wonyansa wa Aamoni,+ akhale osayenera kulambirako.
-