16 Iwo anapita kwa Balamu nʼkukamuuza kuti: “Balaki mwana wa Zipori wanena kuti, ‘Musalole kuti china chilichonse chikulepheretseni kubwera kwa ine, 17 chifukwa ndidzakupatsani mphoto yaikulu, ndipo ndidzachita chilichonse chimene mungandiuze. Chonde tabwerani mudzatemberere anthuwa.’”