-
Numeri 25:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, ataona zimenezi nthawi yomweyo ananyamuka pakati pa gululo nʼkutenga mkondo* mʼdzanja lake. 8 Iye anathamangira mwamuna wa Chiisiraeli uja mpaka kukalowa mutenti yake ndipo anabaya onse awiriwo ndi mkondowo. Anabaya mwamuna wa Chiisiraeli uja limodzi ndi mkaziyo, mpaka mkondowo unakadutsa kumaliseche kwa mkaziyo. Atatero mliriwo unaleka pakati pa Aisiraeli.+
-