12 “Ukamachita kalembera wa ana a Isiraeli,+ aliyense azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi imene ukuwawerengayo. Azichita zimenezi kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.
2 “Uwerenge+ gulu lonse la Aisiraeli* mogwirizana ndi mabanja awo, potengera nyumba za makolo awo, nʼkulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi.