-
Genesis 38:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kumeneko Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanani+ ndipo anamukwatira. Munthuyo dzina lake anali Sua. 3 Mkaziyo anakhala woyembekezera. Kenako, anabereka mwana wamwamuna, ndipo Yuda anamupatsa dzina lakuti Ere.+ 4 Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina lakuti Onani.
-