10 Pa tsiku limene munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe, Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ nʼcholinga choti aphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhale ndi moyo padzikoli komanso kuti aphunzitse ana awo.’+