7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino,+ dziko la mitsinje ya madzi, akasupe ndi madzi ochuluka amene akuyenda mʼzigwa ndi mʼdera lamapiri, 8 dziko la tirigu, balere, mphesa, mitengo ya mkuyu ndi makangaza,+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+