-
Yoswa 1:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Akazi anu ndi ana anu atsale limodzi ndi ziweto zanu kutsidya lino la Yorodano,+ pamalo amene Mose wakupatsani. Koma asilikali amphamvu nonsenu,+ muwoloke ndipo muzikayenda patsogolo pa abale anu,+ mutakonzeka kumenya nkhondo. Muyenera kuwathandiza. 15 Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakatenga malo amene Yehova Mulungu akuwapatsa, mʼpamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kumalo anu amene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani, tsidya lino la Yorodano, kumʼmawa kuno.’”+
-