-
Yoswa 17:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Poyankha, Yoswa anauza anthu a fuko la Yosefe, omwe ndi ana a Efuraimu ndi Manase, kuti: “Ndinu ambiri ndipo ndinu amphamvu kwambiri. Simuyenera kukhala ndi gawo limodzi lokha,+ 18 koma mutengenso dera lamapiri.+ Ngakhale kuti ndi lankhalango, mudzagwetsamo mitengo ndipo gawo lanu likathera kumeneko. Mudzathamangitsa Akanani ngakhale kuti ndi amphamvu ndipo ali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.”+
-