32 Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+
Imbani nyimbo zotamanda Yehova, (Selah)
33 Imbirani iye amene wakwera pamwamba pa kumwamba,+ kumene kwakhalapo kuyambira kalekale.
Mawu ake amphamvu amamveka ngati bingu.
34 Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+
Ulemerero wake uli pa Isiraeli,
Ndipo amasonyeza mphamvu zake kuchokera kumwamba.