Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

      Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu?

      Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+

  • 2 Samueli 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Nʼchifukwa chake ndinudi wodabwitsa,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Palibe amene angafanane ndi inu+ komanso palibe Mulungu wina koma inu nokha.+ Zonse zimene tamva zikutsimikizira zimenezi.

  • 1 Mafumu 8:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Atatero anati: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Mumasunga pangano komanso mumasonyeza chikondi chokhulupirika+ kwa anthu amene amakutumikirani ndi mtima wawo wonse.+

  • Salimo 86:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+

      Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+

  • Yeremiya 10:6, 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Palibe aliyense amene angafanane ndi inu Yehova.+

      Inu ndinu wamkulu ndipo dzina lanu ndi lalikulu komanso lamphamvu.

       7 Kodi ndi ndani amene sakuyenera kukuopani, inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa.

      Chifukwa pakati pa anzeru onse a mʼmitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse,

      Palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena