1 Mose mtumiki wa Yehova atamwalira, Yehova anauza Yoswa+ mwana wa Nuni, mtumiki+ wa Mose, kuti: 2 “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodano ndi kulowa mʼdziko limene ndikulipereka kwa Aisiraeli.+