22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ omwe ndi Aanaki.*+ Mzinda wa Heburoni unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani wa ku Iguputo usanamangidwe.
33 Tinaonakonso Anefili,* ana a Anaki+ omwe ndi mbadwa za Anefili, moti tikadziyerekezera ndi iwowo, ifeyo timangooneka ngati tiziwala. Iwonso ndi mmene amationera.”