-
Yesaya 56:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Izi nʼzimene Yehova wanena kwa anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa. Amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo komanso amene amatsatira pangano langa:
5 “Mʼnyumba mwanga ndiponso mkati mwa mpanda wanga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso ndiponso dzina,
Zomwe ndi zabwino kwambiri kuposa ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina limene lidzakhalapo mpaka kalekale,
Dzina limene silidzatha.
-