-
2 Mbiri 25:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno ufumu wakewo utangokhazikika, anapha atumiki ake amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+ 4 Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo, mʼbuku la Mose, pamene Yehova analamula kuti: “Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita. Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+
-