-
Deuteronomo 4:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Kodi pali anthu enanso amene anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pamoto ngati mmene inuyo munawamvera nʼkukhalabe ndi moyo?+ 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukatenga mtundu wa anthu kuti ukhale wake kuchokera pakati pa mtundu wina pogwiritsa ntchito ziweruzo,* zizindikiro, zodabwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula komanso zinthu zoopsa+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona?
-