-
Deuteronomo 14:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zanu zonse mʼchaka chachitatucho, ndipo muzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu.+ 29 Ndiyeno Mlevi, amene sanapatsidwe gawo kapena cholowa ngati inuyo, komanso mlendo, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye amene akukhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita.”+
-