18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+
3 Ukhale ngati mlendo mʼdzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbira kwa bambo ako Abulahamu+ kuti: