-
Numeri 21:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Choncho Aisiraeli analanda mizinda yonseyi nʼkuyamba kukhala mʼmizinda yonse ya Aamori+ ku Hesiboni ndi mʼmidzi yake yonse yozungulira. 26 Anayamba kukhala kumeneko chifukwa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni, mfumu ya Aamori, amene anamenyana ndi mfumu ya Mowabu nʼkulanda dziko lake lonse mpaka kukafika kuchigwa cha Arinoni.
-