-
Yoswa 18:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka akumpoto kwa Beti-hogila,+ nʼkukathera kugombe lakumpoto kwa Nyanja Yamchere,*+ kumapeto kwa mtsinje wa Yorodano mbali yakumʼmwera. Awa anali malire akumʼmwera a gawo la Benjamini. 20 Kumʼmawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.
-