Yoswa 9:16, 17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo ankakhala pafupi, mʼdera lomwelo. 17 Aisiraeliwo ananyamuka nʼkukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibiyoni,+ Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-yearimu.+ 2 Samueli 6:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka nʼkupita ku Baale-yuda kuti akatenge Likasa la Mulungu woona.+ Pa likasa limeneli anthu amaitanirapo dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ 1 Mbiri 13:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali mʼdera la Yuda kukatenga Likasa la Mulungu woona, Yehova, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Pa Likasa limeneli, anthu amaitanirapo dzina lake.
16 Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo ankakhala pafupi, mʼdera lomwelo. 17 Aisiraeliwo ananyamuka nʼkukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibiyoni,+ Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-yearimu.+
2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka nʼkupita ku Baale-yuda kuti akatenge Likasa la Mulungu woona.+ Pa likasa limeneli anthu amaitanirapo dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+
6 Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali mʼdera la Yuda kukatenga Likasa la Mulungu woona, Yehova, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Pa Likasa limeneli, anthu amaitanirapo dzina lake.