22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ omwe ndi Aanaki.*+ Mzinda wa Heburoni unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani wa ku Iguputo usanamangidwe.
10 Choncho fuko la Yuda linapita kukamenyana ndi Akanani amene ankakhala ku Heburoni, (poyamba dzina la mzinda wa Heburoni linali Kiriyati-ariba). Iwo anapha Sesai, Ahimani ndi Talimai.+